
CHISILAMU NDI CHIPEMBEDZO CHA MBUYE WA ZOLENGEDWA ZONSE
M'dzina la Allah wa chifundo chambiri wa chisoni chosatha
CHISILAMU NDI CHIPEMBEDZO CHA MBUYE WA ZOLENGEDWA ZONSE
Kodi mbuye wako ndi ndani?
Ili ndi funso lalikulu pa dziko la pansi lino; ndipo ndi funso lofunika kuti munthu alidziwe yankho lake.
Mbuye wathu ndi Mulungu amene adalenga mitambo ndi nthaka,ndikumasisa madzi a mvula kuchokera ku mwamba,ndipo kuchokera mu madzi amenewo amameretsa ndikumatulutsa zipatso,kumeretsa mitengo yomwe imatulutsa zakudya zathu ndi nyama,yama zake zimene ifenso timadya. Iye ndi Mulungu amene adalenga ife komanso makolo athu,komanso adalenga kena kalikonse. Ameneyo ndi Mulungu amene adaika usana ndi usiku,komanso yemweyo ndiye adauchita usiku kukhala nthawi yopuma ndikugona,komanso adauchita usana kukhala ofunafuna chakudya ndi zosowa zapa moyo. Iye ndi Mulungu amene adatifewetsera ife dzuwa,mwezi,nyenyezi,nyanja,ndikutifewetseranso ife nyama zomwe timadya nyama yake,ndipo timapindulanso pokumwa mkaka ochokera mu nyama zimenezi,ndikumapangira nsapato komanso ulusi kuchokera mu zikopa zake.
Kodi mbiri za mbuye wa zolengedwa zonse ndi ziti?
Ambuye Mulungu ndi amene adalenga zolengedwa zonse, ndipo iye ndi amene amaziongolera zolengedwa ku zinthu zoona ndi njira yowongoka. Iye ndi amene amayendetsa zonse zokhuza cholengedwa chilichonse,amazipasa zolengedwa zonse zosowa zawo,ndipo iye ndi mwini kena kalikonse pa dziko lino komanso umoyo omwe ukubwera,ndipo kanthu kena kalikonse kupatula iye mwini ndi kake. Iye ndi Mulungu amene ali ndi moyo osatha amene sadzamwalira komanso samagona,ndipo iye ndi odaliridwa amene kudzera mwa iye zolengedwa zonse zimapeza zosowa za pamoyo, ndipo iye ndi Mulungu amene chisoni chake chimakhuza cholengedwa chilichonse, ndipo iye ndi Mulungu amene palibe chinthu chimabisika kwa iye pano pa dziko lapansi komanso kumwamba. Palibe kalikonse kofanana ndi iye,ndipo iye ndi okumva,komanso iye amaona kalikonse, ndipo iye ali pa mwamba pa zolengedwa zonse,ndipo safuna thandizo kuchokera ku zolengedwa zake,pomwe zolengedwa zake zimasowa thandizo lake,iye samalowa m'matupi mwa zolengedwa zake,ndiponso palibe cholengedwa chilichonse chimasanduka iye Mulungu,mwini mphamvu zonse. Ambuye Mulungu ndi amene adalenga dziko limeneli lomawoneka ndi ndondomeko yabwino yofanana popanda kusiyana kaya ndi ndondomeko ya m'thupi la mu munthu kapena chinyama kaya ndondomeko ya mmene dziko lazungulilila ndi dzuwa lake nyenyezi zake ndi zina zilizonse zomwe zilipo.
Ndipo kena kalikonse komwe kamapembedzedwa posakhala Mulungu m'modzi,kalibe mphamvu zozipatsa zokha zabwino kapena zowawa, ndiye zitheka bwanji kuti zipereke zabwino kwa amene akuchipembedzayo,kapena kumuchosera vuto ochipembedzayo akakhala ndi vuto.
Kodi zoyenera kuti ife timuchitire mbuye wathu ndi ziti?
Zoyenera kuchitiridwa ndi anthu onse ndikumupembedza iye yekha ndikuti asamuphatikize ndi kena kalikonse. Anthu sakuyenera kupembedza kena kalikonse kusiya iye Mulungu ,kapena asamupembedze iye momuphatikiza ndi munthu aliyense,kapena mwala,kapena mtsinje,kapena chilichonse chopanda moyo,kapena nyenyezi,kapena chinachilichonse. Koma akuyenera kuti mapemphero onse achitike pofuna kusangalatsa iye yekha mbuye wa zolengedwa zonse.
Kodi zoyenera Mulungu kuwachitira anthu ndi ziti?
Zoyenera Mulungu kuwachitira anthu ngati anthuwo akumupembedza Mulungu m'modzi yekha,ndikuti Mulungu awakhazika umoyo wabwino pa dziko pano,momwe azikhala akupedza mtendere ,samakhala ndi mantha ena alionse,adzikhala umoyo odekha ndi osangalala ndi zomwe Mulungu wapatsa. Ndipo moyo omwe ukubwera,akawalowesa ku minda ya mtendere,komwe kuli mtendere okhazikika komanso akakhala kumeneko mpaka kalekale. Koma ngati anthu atamunyoza Mulungu ndikumasemphana ndi Malamulo ake,Mulungu amaupanga moyo wawo kukhala opweteka ndi odzadzana ndi madandaulo,ngakhale akumaganiza ndikumaziona eni akewo kuti ali pa mtendere ndi mpumulo.Ndipo moyo omwe ukubwera akawalowesa ku moto,komwe sakatulukako,ndipo adzakhala ndi zilango zosatha mpaka kalekale , ndipo adzakhala ku motoko moyo wawo onse osatulukako.
Kodi tikupedzeka pa dziko pano chifukwa chani?Nanga tinalengedwa chifukwa chani?
Mulungu olemekezeka watiuza kuti iyeyo adatilenga ife pa chifukwa cholemekezeka; chomwe ndikumupembedza iye yekha,ndikuti tisamamuphatikize ndi china chilichonse. Komanso adatipatsa ulamuliro oyang'anira dziko la pansi pogwira ntchito yabwino ndikumakonza zinthu zomwe zasokonekera. Kwa munthu amene angamapembedze Mulungu wina posakhala Mlengi wake,ndiye kuti sakudziwa cholinga chomwe adalengedwera,komanso sadachite zoyenera kumuchitira mbuye wake,ndipo kwa munthu amene angamaononge pa dziko la pansi,ndiye kuti sakudziwa za ntchito yomwe anapasidwa.
Kodi tingamupembedze bwanji mbuye wathu?
Mbuye wathu Mulungu olemekezeka sadangotilenga ndikutisiya osatipasa malamulo , ndipo sadauchite umoyo wathu kukhala omangosewera. Koma kuti kuchokera mwa anthu,adasankha ena ndikuwachita kukhala atumiki kwa anthu awo, omwe(atumikiwo)adali anthu okwanira makhalidwe awo,oyera mitima,olungama. Mulungu adawatumizira atumikiwa uthenga wake, ndipo mkati mwa uthengawo adaikamo maphunziro owadziwitsa anthu zokhuza mbuye wawo olemekezeka, komanso zokamba zakuukitsidwa kwa anthu kuti akaime pamaso pa mbuye wawo tsiku la chiweruzo lomwe ndi tsiku lowerengesera ntchito za anthu ndikuwapatsa malipiro. Ndipo atumiki a Mulungu adafikitsa uthenga wa mbuye wawo kwa anthu awo, powafotokozera momwe angapembedzere mbuye wawo, ndipo adawafotokozera anthu awowo m'mene ndondomeko za mapempherowo zimakhalira, nthawi zopemphelera,komanso malipiro ake pa dziko pano, komanso moyo omwe ukubwera. Komanso atumikiwa adawaletsa anthu awo zomwe mbuye wawo adawaletsa anthuwo, mu zakudya, zakumwa ndi ma ukwati. Ndipo atumikiwa adawasonyeza anthu awo ku makhalidwe abwino apamwamba, ndikuwaletsa makhalidwe oipa.
Kodi chipembedzo chomwe chikalandiridwe kwa Mulungu ndi chiti?
Chipembedzo chomwe chikalandiridwe pa maso pa Mulungu ndi chisilamu,ndipo chimenecho ndi chipembedzo chomwe adabwera nacho atumiki onse, ndipo tsiku la chiweruzo,Mulungu sakalandira chipembedzo china posakhala cha chisilamu. Chipembedzo china chilichonse chomwe anthu angamachitsatire posakhala chisilamu, ndi chipembedzo chosokonekera, ndipo sichikamuthandiza mwini wakeyo. Pa dziko pano azikhala umoyo opweteka ndi wa tsoka komanso moyo omwe ukubwera akhala umoyo wamazunzo.
Kodi mapata achisilamu ndi nsichi zake ndi ziti?
Ichi ndi chipembedzo chomwe Mulungu adawapepusira akapolo ake malamulo achipembedzochi. Nsichi yaikulu ya chisilamu ndikuti munthu ukhulupilire mwa Mulungu kukhala mbuye komanso opembedzedwa mwa chooandi,komanso ukhulupilire mwa angelo ake,mabuku ake,atumiki ake,tsiku lotsiriza ndi chikonzero cha Mulungu pa zochitika zapa moyo. Munthu uikire umboni kuti palibe Mulungu oyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Mulungu m'modzi yekha,ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi mtumiki wa Mulungu,kupemphera kasanu pa tsiku,kupereka cha ulere(zakat) kamodzi pa chaka ngati uli ndi chuma choyenera kuperekera chaulere,kusala kudya omwe ndi umodzi pa chaka,kukachita mapemphero a hajj ku nyumba ya Mulungu mu mzinda wa makkah yomwe adaimanga Abraham motsatira lamulo la Mulungu,ngati uli ndikuthekera kotero. Ndikumapewa zomwe Mulungu adakuletsa,monga kumuphatikiza ndi zinthu zina, kupha munthu popanda chifukwa chovomerezeka pa chipembedzo, kuchita chiwerewere,kudya chuma choletsedwa. Ukakhulupilira mwa Mulungu, ndikumagwira ntchito zabwinozi, ndikumapewa zinthu zoletsedwazi, ndekuti iwe ukhala msilamu weni weni pa dziko pano,ndikuti pa tsiku lotsiriza, Mulungu akamupatsa mtendere osatha, ndipo akakhala ku malo amtendere mpaka kale kale.
Kodi chipembedzo cha chisilamu ndi chipembedzo cha gulu la anthu opatulika kapena mtundu wa anthu opatulika?
Chisilamu ndi chipembedzo cha Mulungu chomwe adachitumiza kwa anthu onse, mu malamulo ake palibe munthu amene amakhala pa mwamba pa nzake,kupatula podzera mukukwaniritsa kuopa Mulungu ndikugwira ntchito yabwino, koma kupatula zimenezo, anthu onse ndi ofanana pa malamulo achisilamu.
Kodi anthu angadziwe bwanji kuyankhula zoona kwa atumiki-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iwo?
Anthu angadziwe kuyankhula zoona kwa atumimiki kudzera mu njira zosiyanasiyana monga:
Kuti zomwe zimabwera ndi atumiki mu zinthu zoona ndi zowaongolera anthu ku njira yowongoka,ndi zinthu zoti nzeru zabwino za munthu ndi chilengedwe cha bwino cha munthu zimazivomereza. Nzeru za bwino zimaikira ubwino kuti uthenga omwe adabwera nawo ndi wabwino, ndipo palibe amene angabwere ndi zinthu ngati zimenezo posakhala atumiki okha.
Kuti zomwe adabwera nazo atumiki, muli malamulo okonza zipembedzo za anthu komanso moyo wawo wa dziko, ndikuongoka kwa zinthu zawo, ndikutukuka kwa maiko awo, komanso kuteteza chipembedzo chawo, nzeru zawo, chuma chawo ndi ulemelero wawo.
Kuti atumkiki-mtendere ukhale pa iwo-samapempha malipiro kwa anthu chifukwa chowasonyeza anthu ku zinthu zabwino ndikuwaongolera ku njira yabwino, koma kuti amadikilira malipiro awo kuchokera kwa mbuye wawo.
Ndithu zomwe adabwera nazo atumiki, ndi zoona ndipo sizinasakanikirane ndi chokaikitsa chilichonse, sizitsutsana kapena kuombana, ndi kuti mtumiki wina aliyense amatsimikiza zomwe atumiki ena anabwera nazo iye asanabwere, ndikumaitanira anthu ku zinthu zofanana ndi zomwe atumiki anali m'mbuyo mwake amaitanira anthu.
Kuti Mulungu amawalimbikitsa atumiki-mtendere ukhale pa iwo -ndi zizindikiro zoonekera,komanso zozizwitsa za mphamvu zomwe Mulungu amawapatsa atumiki;kuti ukhale umboni wakuyankhula kwawo zoona kuti iwowo ndi atumiki ochokera kwa Mulungu, ndipo chozizwitsa chachikulu kwambiri mu zozizwitsa za atumiki, ndi chozizwitsa chomwe adapastidwa mtumiki otsiriza Muhammad-mtendere ndi madalitso a Mulungu zikhale pa iye-, yomwe ndi Qur'an yolemekeza.
Kodi Qur'an yolemekezeka ndi chiyani?
Qur'an yolemekezeka limenelo ndi buku la mbuye wa zolengedwa zonse, amenewo ndi mau a Mulungu omwe adatsika nawo m'ngelo Gabriel-mtendere ukhale pa iye-kupita nawo kwa mtumiki Muhammad (SAW); ndipo mu buku limeneli muli zonse zomwe Mulungu walamulira anthu kuti azidziwe zokhuza Mulungu, Angelo ake, mabuku ake, atumiki ake, tsiku lotsiriza, ndi zikonzero za Mulungu zabwino ndi zoipa. Mu buku limeneli,mulinso malamulo okakamiza kupembedza Mulungu,komanso mwatchulidwa zinthu zoletsedwa zomwe zikukakamizidwa kuzisiya,komanso mwatchulidwa makhalidwe abwino ndi oipa, ndi zonse zokhuza chipembedzo cha anthu ndi zonse za moyo wawo wa dziko lapansi, ndi moyo wawo omwe ukubwera. Limenelo ndi buku lozizwitsa lomwe Mulungu adawauza anthu okanira a nthawi ya mtumiki kuti abweretse buku lofanana ndi ilolo, ndipo buku limeneli lidzakhala likutetezedwa mu chinenero chomwe idatsika nacho popanda kuchosamo ngakhale chilembo chimodzi kufikira tsiku lotsiriza, ndipo palibe ngakhale liwu limodzi lomwe lidzasinthidwe.
Kodi umboni oti anthu adzaukitsidwa m'manda ndikukawerengetseredwa ntchito zawo ndi uti?
Kodi iwe sumaiona nthaka ikakhala youma kuti imakhala yokufa, imakhala ilibe moyo? ndipo madzi a mvula akagwera pamwamba pake, imasweka ndikumeretsa zomera zosiyanasiyana? Mulungu amene amaidzutsa nthaka, ndi Mulungu wake yemweyo amene adzakwanitse kudzutsa anthu okufa kuchokera m'manda mwawo. Ndithu Mulungu amene adalenga munthu kuchokera ku dontho la madzi onyozeka, Mulungu ameneyo ali ndi mphamvu zozamudzutsa munthuyo tsiku la chiweruzo, kenako ndikukamuwerengesera ntchito zake, ndikukamupatsa malipiro ake okwanira,ngati anagwira ntchito yabwino, ndiye kuti akapeza zabwino, ngati anagwira ntchito zoipa, akapezanso zoipa. Mulungu amene adalenga mitambo, nthaka ndi nyenyezi, ndi okutha kumubwezeresa munthu kukhalanso wa moyo; chifukwa choti kubwezeretsa kulenga munthu kachiwiri, ndikopepuka kuposa kulenga mitambo ndi nthaka.
Kodi tsiku lotsiriza kudzakhala chiyani?
Mulungu adzawadzutsa anthu kuchokera m'manda mwawo, kenako adzawawerengesera ntchito zawo zomwe amagwira dziko la pansi. Kwa munthu amene adakhulupilira ndikuwavomereza atumiki, Mulungu akamulowetsa munthuyo ku mtendere, komwe kuli mtendere okhazikika omwe palibe munthu anaganizapo m'mene ulili chifukwa chakukula kwake mtenderewo. Kwa munthu amene angakanire mwa Mulungu, akamulowetsa ku moto, komwe kuli zilango zosatha, zomwe munthu sanayambe ataziganizira momwe zilili. Ndipo munthu akakalowa ku mtendere kapena ku moto, sakamwalirako mpaka kale kale , ndipo akakhala pa mtendere kapena pa zilango mpaka kale kale.
Achite chiyani munthu akafuna kulowa chisilamu? kodi pali miyambo yofunika kuchita?kapena pali anthu olemekezeka ofunika kwapempha kaye chiloledzo?
Munthu akadziwa kuti chisilamu ndi chipembedzo choona, ndi kuti chisilamu ndi chipembedzo cha mbuye wa zolengedwa zonse, chofunika kwa munthu ameneyo ndikufulumira kulowa chisilamu; chifukwa munthu wa nzeru amati choona chikadziwika kwa iye, amayenera kufulumira kuchitsatira, ndipo sakuyenera kuchedwetsa kulowa chisilamu. Munthu amene akufuna kulowa chisilamu, sizoyenera kuchita mwambo wapadera, kapena kuti papezeka munthu wamkulu olemekezeka kuti amuloleze ndikuonelera kulowa kwake mchisilamu, koma kuti ngati patapezeka msilamu kapena kulowa chisilamu pa malo omwe amachitika zinthu za chisilamu, izo ndi zabwinonso, koma ngati palibe msilamu kapena malo achisilamu oti iyeyo mkulowera chisilamu malo amenewo, ndi zokwanira kungoyankhula mau awa: (Ndikuikira umboni kuti palibe Mulungu opembedzedwa mwa choonadi koma Mulungu m'modzi yekha, komanso ndikuikira umboni kuti Muhammad ndi mtumiki wa Mulungu), ayankhule mau amenewa akudziwa matanthauzo ake, komanso akukhulupilira matanthauzowo, akatero amakhala msilamu; kenako adziphunzira malamulo ena achisilamu pang'ono pang'ono; kuti adzichita moyenera zomwe Mulungu wamulamulira kuti adzichita.
Kuti mudziwe zambiri: https://byenah.com/ny