CHISILAMU
2
CHISILAMU
Chipembedzo chogwirizana ndi chilengedwe, nzeru ndi
chobweresa chisangalalo.
M'dzina la Mulungu ,Wachifundo Chambiri ,Wachisoni Chosatha.
Kodi unayamba wazifunsa wekha?
Kodi ndi ndani amene adalenga mitambo ndi nthaka,komanso
zolengedwa zazikulu zikupezeka ku mitambo ndi pansi pa nthaka? Kodi
ndani adapanga ndondomeko yokuya ndi yokonzedwa mwa ukadaulo?
Kodi dziko lalikululi zimatheka bwanji zinthu kuchitika mwa
ndondomeko komanso mokhazikika potengera malamulo okuya omwe
akhala akulitetedza dzikoli kwa zaka zochuluka?
Kodi Dzikoli lidazilenga lokha? Kapena zinachokera pachabe? Kapena
zinangopezeka mwangozi?
Ndani adakulenga iwe?
Kodi ndi ndani amene adaika ndondomeko yodzama mu ziwalo za pa
thupi pako komanso ziwalo za zinyama za moyo?
Palibe amene angavomereze kuuzidwa kuti nyumbayi idabwera
popanda wina kumanga! Kapena kumuuza kuti nyumbayi ilibe yemwe
anaibweretsa! Kodi anthu ena angakhulupirire bwanji anthu amene
amanena kuti chilengedwe chonsechi chinabwera popanda Mlengi? Kodi
munthu woganiza bwino angavomereze bwanji kuuzidwa kuti dongosolo
lolondola lachilengedwechi linangopezeka mwangozi?
Ndithu, kuli Mulungu wamkulu, Mlengi ndi Wolamulira wa
chilengedwe chonse ndi zonse zili m’menemo, ndipo Iye ndi Mulungu
Wamphamvu zonse.
Ndipo Ambuye, Ulemelero ukhale kwa Iye, adatitumizira ife atumiki,
ndipo adawatsitsira atumikiwo mabuku (chivumbulutso),ndipo lotsiriza
mwa mabukuwo ndi buku la Qur’an lolemekezeka, limene Mulungu
adalivumbulutsa kwa Muhammad, womaliza mwa atumiki a Mulungu,
ndipo kudzera mwa mabuku ake ndi atumiki ake:
⦁Anatizindikiritsa ife za iye mwini, mbiri zake, ndi zoyenera kuti
tizimuchitira, ndipo wafotokoza zoyenera iye kutichitira ife ngati tachita
zoyenera kumuchitira iyeyo.
3
⦁Watisonyeza potidziwitsa kuti iye ndi Mbuye amene adalenga
zolengedwa zonse, ndikuti iye ndi wa moyo mpaka kale sadzamwalira,
ndipo zolengedwa zonse zili m’manja mwake,pansi pa mphamvu ndi
ulamuliro wake.
Ndipo adatiuza kuti zina mwa mbiri zake ndi kudziwa, ndithu iye
ngodziwa chilichonse, ndi kuti ngwakumva,kupeya ,ndipo palibe chobisika
kwa iye padziko lapansi kapena kumwamba.
Ndipo Mbuye ndi wamoyo wamuyaya, okhazikika, amene mwa Iye
yekha ndi m'mene moyo wa cholengedwa chilichonse umachokera,
Ulemelero ukhale kwa Iye, ndipo ndi yemwe mwa iye wakhazikika moyo
wa zolengedwa zonse, Ulemelero ukhale kwa iye wamphamvu zonse adati:ُ
(Palibe Mulungu opembedzedwa mwa choonadi koma iye, wamoyo
wamuyaya,odaliridwa ndi zolengedwa zonse,samasinza kapena kumupeza
tulo,zolengedwa zonse zili ku mwamba ndi dziko lapansi zili m'manja
mwake,palibe amene angakhale ndi mphamvu zomuthandiza wina pamaso
pa Mulungu kupatula Mulungu ataloleza kuti zitero,amadziwa za
zolengedwa zonse zomwe zinalipo kalekale,zomwe zili pano ndi zomwe
zidzalengedwe msogolo,amadziwa za msogolo zomwe zidzachitikire
zolengedwa zake komanso zomwe zinachitika kale,palibe cholengedwa
chimadziwa zobisika zake kupatula zomwe iye Mulungu wachidziwitsa
cholengedwacho,mpando wa ufumu wake malo ake ndi akulu monga
m'mene kulili kumwamba ndi dziko lapansi,ndipo sizimamulemera
kuzisunga ndikuteteza kumwamba ndi dziko lapansi,iye Mulungu ndi
wapamwamba komanso wamkulu). [Suratu Al-Baqara:255]
4
⦁Ndipo adatiuza kuti Iye ndi Ambuye, amene amadziwika ndi mbiri
zangwiro, ndipo adatipatsa maganizo ndi mphamvu zomwe zimazindikira
zodabwitsa za chilengedwe Chake ndi mphamvu zake, zomwe
zimatisonyeza ukulu wake, mphamvu zake, ndi ungwiro wa mbiri zake.
ndipo anaika mwa ife chibadwa chimene chimasonyeza ungwiro Wake ndi
kuti Iye sangadziŵike ndi kupunguka.
⦁Ndipo anatiphunzitsa kuti Ambuye ali pamwamba pa mitambo yake,
ndipo salowa m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi silikhala mwa Iye.
⦁Ndipo anatiuza kuti tiyenera kugonjera kwa Iye, Ulemerero ukhale
kwa Iye, pakuti Iye ndiye Mlengi wathu ndi Mlengi wa dziko komanso
muyendetsi wake
Mlengi ali ndi mbili za ukulu ndipo sangadziŵike konse ndi kusoŵa
kapena kupereŵera, Mbuye saiwala, samagona, sadya chakudya, ndipo
sangakhale ndi mkazi kapena mwana. Zolemba zonse zomwe zili ndi
chilichonse chotsutsana ndi ukulu wa Mlengi, sizili mbali ya chivumbulutso
cholondola chomwe chidadza ndi Atumiki a Mulungu, mtendere ukhale pa
iwo.
Mulungu adanena mu buku la Quran kuti:ۡ
(Nena -iwe Mtumiki -SAW- kwa amene akukufunsa mwachipongwe,
mbiri za Mulungu wako-kuti Iye ndi Mulungu m'modzi, (alibe nzake),
Mulungu ndi wokhala ndi zonse wodaliridwa ndi zolengedwa zake.
sadabale (mwana) ndiponso sadaberekedwe.
ndiponso palibe aliyense wofanana ndi iye. [Al-Ikhlas:1-4].
Ngati mumakhulupirira kuti kuli Mulungu Mlengi...kodi munayamba
mwadzifunsapo kuti cholinga cha chilengedwe chanu chinali chiyani? Kodi
Mulungu amafuna chiyani kwa ife, ndipo cholinga cha kupezeka kwathu
n’chiyani?
5
Kodi n’kutheka kuti Mulungu anatilenga n’kutisiya osasamala? Kodi
zingakhale kuti Mulungu analenga zolengedwa zonsezi popanda
chifukwa kapena cholinga?
Zoona zake n’zakuti, Mbuye, Mlengi Wamkulu, “Mulungu,” anatiuza za
cholinga chake pakulengedwa kwa ife, chomwe ndi kupembedza Mulungu
yekha, ndi zimene amafuna kwa ife! ndipo Adatiuza kuti Iye yekha ndiye
woyenera kupembedzedwa, ndipo adatifotokozera kudzera mwa atumiki
ake, mtendere ukhale pa iwo, momwe tingamupembedzere? Kodi
tingaziyandikitse bwanji kwa Iye potsatira malamulo Ake ndi kusiya
zoletsa zake? Kodi tingapeze bwanji chiyanjano Chake? Timachenjeza za
chilango chake, ndikutiuza za tsogolo lathu pambuyo pa imfa?
Ndipo Adatiuza kuti moyo wapadziko lapansi ndi mayeso chabe, ndi
kuti moyo weniweni ndi wokwanira udzakhala m’moyo wapambuyo pa
imfa.
Adatiuzanso kuti yemwe adzapembedza Mulungu monga momwe
adamulamulira, nasiya zomwe adamuletsa. Adzakhala ndi moyo wabwino
padziko lapansi ndi chisangalalo chamuyaya tsiku lomaliza, ndipo amene
samumvera ndi kukanira iye adzapeza masautso padziko lapansi ndi
chilango chamuyaya tsiku lomaliza.
Chifukwa tikudziwa kuti sitingadutse moyo uno popanda aliyense
mwaife kulandira mphotho ya zomwe adachita, zabwino kapena
zoyipa; ndiye sipadzakhala chilango kwa ochita zoipa, komanso
malipiro abwino kwa ochita zabwino?
Ndipo ndithu Mbuye wathu watiuza kuti munthu akakhale opambana
tsiku lotsiriza popeza chisangalalo cha Mulungu, ndi kupulumuka ku
chilango chake sizingatheke popanda kulowa chisilamu,komwe ndi
kugonjera mwa Iye Mulungu ,kumupembedza iye yekha popanda
omuphatikiza naye, kugonjera Iye pomvera, ndi kutsatira malamulo ake
mwa nsangala ndikuvomera, ndiye watiuzanso kuti pa tsiku la chiweruzo
iye sadzalandira chipmbedzo china kuchokera kwa anthu chosakhala
chisilamu, Mulungu adanena kuti:
(Ndipo amene angatsate Chipembedzo china chosakhala Chisilamu,
sichidzalandiridwa kwa iye, ndipo iye tsiku lomaliza adzakhala mmodzi
mwa anthu otaika [Al-Imran: 85].
Amene ayang’ana zimene anthu ambiri akupembedza lero; ampeza
wina akupembedza munthu, wina akupembedza fano, wina akupembedza
Nyenyezi, ndi zina zotero.Ndipo sizoyenera kwa munthu wanzeru
kupembedza zina koma Mbuye wa zolengedwa zonse, wokwanira mu
mbiri zake, nanga apembedza bwanji cholengedwa ngati iye mwini kapena
chapansi kuposa iye! Mulungu wopembedzedwa sangakhale munthu, fano,
mtengo, kapena nyama!
Zipembedzo zonse zomwe anthu akuzipembedza lero - kupatula
Chisilamu - nzosavomerezeka kwa Mulungu, chifukwa ndi zipembedzo
zopangidwa ndi anthu, kapena zipembedzo zomwe zidali zamulungu
kenako nkusokonezedwa ndi manja a anthu, pomwe chisilamu ndi
chipembedzo cha Mbuye wa Zolengedwa zonse, sichingasinthe kapena
kusinthika, ndipo buku la chipembedzochi ndi Qur’an yopatulika, ndi buku
losungidwa monga momwe Mulungu adalivumbulutsira ndipo likadali
m’manja mwa Asilamu mpaka lero m’chinenero chomwe
lidavumbulutsidwa nacho kwa Mtumiki womaliza.
Chimodzi mwa maziko a Chisilamu ndi kukhulupilira atumiki onse
amene Mulungu anawatuma, onsewo adali anthu, Mulungu adawapatsa
zisonyezo ndi zozizwitsa, ndipo adawatumiza kuti aitanire anthu kuti
apembedze Iye yekha, popanda ophatikizana nawo. Womaliza mwa
azithenga ake ndi M'thenga Muhammad (SAW) Mulungu adamutumiza ndi
lamulo lomaliza lomwe limafafaniza malamulo a atumiki amene adalipo
patsogolo pake, ndipo adamuthandiza ndi zizndikiro zazikulu ndipo
chachikulu kwambiri ndi Qur'an yopatulika, liwu la Mbuye wa zolengedwa
zonse, Buku lalikulu kwambiri lodziwika kwa anthu, lozizwitsa m'menemo,
m'mawu ake, dongosolo lake, malamulo ake, ndipo m'menemo muli
chiongoko cha kuchoonadi chobweretsa chisangalalo Padziko lino lapansi
ndi tsiku lomaliza ndipo ndithu idavumbulutsidwa m’Chiarabu.
Pali maumboni ambiri omveka kuchokera mu nzeru ngakhale
maphunziro omwe akutsimikizira popanda chikaiko kuti Qur’an iyi ndi
mawu a Mlengi, Ulemerero ukhale kwa Iye, ndikuti sizingatheke kukhala
zonena za anthu.
Zina mwa maziko a Chisilamu ndi kukhulupirira angelo ndi
kukhulupirira tsiku lomaliza, pamene Mulungu adzaukitsa anthu m’manda
7
awo pa tsiku lachimaliziro kuti awawerengere pazochita zawo, choncho
amene anachita zabwino ali wokhulupirira adzapeza chisangalalo
chosatha ku m’Paradaiso, ndipo amene Akanira ndi kuchita zoipa,
adzakhala ndi chilango chachikulu ku moto. ndipo mwa maziko a
Chisilamu ndiko kukhulupilira zimene Mulungu adakonza nzabwino
kapena zoipa.
Ndipo Chipembedzo cha Chisilamu ndi njira yokwanira ya umoyo,
yogwirizana ndi Chilengedwe ndi nzeru, ndipo chimalandiridwa ndi
mitima yangwiro, idakhazikitsidwa ndi Mlengi Wamkulu pa zolengedwa
Zake, ndipo ndi chipembedzo cha ubwino ndi chisangalalo kwa anthu onse
padziko lapansi ndi tsiku lomaliza, silisiyanitsa gulu la munthu wina ndi
wina, ngakhalenso mtundu wina kuposa wina, ndipo anthu m’menemo
ndiwofanana, palibe amene ali wopatulika mu Chisilamu kupatula ndi
mulingo wa ntchito zake zolungama.
Mulungu wapamwamba adenena:ۡ
(amene akuchita zabwino, wamwamuna kapena wamkazi uku ali
msilamu timkhazika ndi moyo wabwino (pano pa dziko, ndi tsiku la
Kiyama) Tidzawalipira malipiro awo mochuluka kwambiri, Chifukwa cha
zabwino zomwe ankachita.) [Al-Nahl: 97].
Zina mwa zimene Mulungu akutsimikiza m’Qur’an yopatulika ndi kuti
kukhulupirira kuti Mulungu ndi Mbuye ndi wopembedzedwa, Chisilamu
ndi chipembedzo, ndi kuti Muhammad ndi Mtumiki, ndi kulowa
m’Chisilamu ndi chinthu chofunikira chomwe munthu alibe kuchitira
mwina, Tsiku lachimaliziro padzakhala chiwerengero ndi malipiro. Amene
ali Msilamu wokhulupirira woona, adzapambana ndi kupambana
kwakukulu. Ndipo amene anali wokanira adzakhala ndi kuluza koonekera.
Mulungu wapamwamba adanena kuti:
(... Ndipo amene angamvere Mulungu ndi Mtumiki wake,
adzamulowetsa m,minda yomwe pansi pake mitsinje ikuyenda. adzakhala
m'menemo muyaya. kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.
Koma amene anganyoze Mulungu ndi Mtumiki wake, ndi kulumpha
malile ake, (Mulungu) adzamulowetsa kumoto; nadzakhala mmenemo
muyaya. ndipo adzapeza chilango chosambula). [Al-Nisa:13-14].
Amene akufuna kulowa m’chisilamu anene kuti:(ddikuikira umboni
kuti palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Mulungu m'modzi yekha
ndipo ndikuikira umboni kuti Muhammad ndi M'thenga wa
Mulungu),podziwa tanthauzo lake ndi kukhulupirira, ndipo m’menemo
amakhala Msilamu. Kenako amaphunzira malamulo ena onse a chisilamu
pang'onopang'ono. Kuti achite zimene Mulungu wamulamula.
kuti mumve zambiri: https://byenah.com/ny
9
CHISILAMU 3
Chipembedzo chogwirizana ndi chilengedwe, nzeru ndi chobweresa
chisangalalo. 3
Ndani adakulenga iwe? 3
Kodi n’kutheka kuti Mulungu anatilenga n’kutisiya osasamala? Kodi
zingakhale kuti Mulungu analenga zolengedwa zonsezi popanda chifukwa
kapena cholinga? 5
Chifukwa tikudziwa kuti sitingadutse moyo uno popanda aliyense mwaife
kulandira mphotho ya zomwe adachita, zabwino kapena zoyipa; ndiye
sipadzakhala chilango kwa ochita zoipa, komanso malipiro abwino kwa
ochita zabwino? 6
10